48 cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.
49 Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;
50 mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamcitira cifundo mwana;
51 ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.
52 Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
53 Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.
54 Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu diso lace lidzaipira mbale wace, ndi mkazi wa pa mtima wace, ndi ana ace otsalira;