15 Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa;
16 popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kusunga malamulo ace ndi malemba ace ndi maweruzo ace, kuti mukakhale ndi moyo ndi kucuruka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.
17 Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukaceteka, ndi kugwadira milungu yina ndi kuitumikira;
18 ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzacuruka m'dziko limene muolokera Yordano kulowamo kulilandira.
19 Ndicititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;
20 kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ace, ndi kummamatira iye, tr pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ocuruka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.