25 Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.
26 Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,Wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,Ndi pa mitambo m'ukulu wace.
27 Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako;Ndi pansipo pali manja osatha.Ndipo aingitsa mdani pamaso pako,Nati, Ononga.
28 Ndipo Israyeli akhala mokhazikika pa yekha;Kasupe wa Yakobo;Akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo;Inde thambo lace likukha mame.
29 Wodala iwe, Israyeli;Akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova,Ndiye cikopa ca thandizo lako,Iye amene akhala lupanga la ukulu wako!Ndi adani ako adzakugonjera; Ndipo udzaponda pa misanje yao.