22 pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordano; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanu lanu.
23 Dzicenjerani, mungaiwale cipangano ca Yehova Mulungu wanu, cimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, cifaniziro ca kanthu kali konse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.
24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.
25 Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikuru m'dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m'cifaniziro ca kanthu kali konse, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace:
26 ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zicite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kucotsedwa ku dziko limene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu; masiku anu sadzacuruka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.
27 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.
28 Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, nchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.