14 koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira nchito iri yonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena buru wako, kapena zoweta zako ziri zonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wanchito wako wamwamuna ndi wanchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.