11 Ndipo Yehova anati kwa ana a Israyeli, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aaigupto ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Aftlisti?
12 Asidoni omwe, ndi Aamaleki, ndi Amidyani anakupsinjani. Pamenepo munapfuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao.
13 Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu yina, cifukwa cace sindikupulumutsaninso.
14 Mukani ndi kupfuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.
15 Koma ana a Israyeli anati kwa Yehova, Tacimwa, muticitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.
16 Pamenepo anacotsa milungu yacilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wace unagwidwa cisoni cifukwa ca mabvuto a Israyeli.
17 Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Gileadi. Ndi ana a Israyeli anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.