13 Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu yina, cifukwa cace sindikupulumutsaninso.
14 Mukani ndi kupfuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.
15 Koma ana a Israyeli anati kwa Yehova, Tacimwa, muticitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.
16 Pamenepo anacotsa milungu yacilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wace unagwidwa cisoni cifukwa ca mabvuto a Israyeli.
17 Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Gileadi. Ndi ana a Israyeli anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.
18 Ndipo anthu, akalonga a Gileadi, ananenana wina ndi mnzace, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? iye adzakhala mkuru wa onse okhala m'Gileadi.