12 Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?
13 Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.
14 Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;
15 nanena naye, Atero Yefita, Israyeli sanalanda dziko la Moabu kapena dziko la ana a Amoni;
16 pakuti pakukwera iwo kucokera ku Aigupto Israyeli anayenda m'cipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;
17 pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.
18 Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.