3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.
4 Cifukwa cace udzisamalire, usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye cinthu ciri conse codetsa;
5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.
6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;
7 koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye ciri conse codetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire mpaka tsiku la kufa kwace.
8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize ico tizicitira mwanayo akadzabadwa.
9 Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwanuna wace Manowa palibe.