1 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kucokera ku Giligala kumka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kucokera ku Aigupto, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola cipangano canga nanu ku nthawi yonse;
2 ndipo inu, musamacita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwacicita ici cifukwa ninji?
3 Cifukwa cacenso ndinati, Sindidzawapitikitsa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.
4 Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israyeli, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.
5 Potero analicha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.
6 Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israyeli anamuka, yense ku colowa cace, dziko likhale lao lao.