8 Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwace, kapena kupambukira nyumba yace,
9 koma tsopano ici ndico tidzacitira Gibeya: tidzaukwerera ndi kulota maere.
10 Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mapfuko onse a Israyeli; ndi zana limodzi pa zikwi cimodzi, ndi cikwi cimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibeya wa Benjamini, aucitire monga mwa copusa conse unacita m'Israyeli.
11 Potero amuna onse a Israyeli anasonkhanira mudziwo, olunzika ngati munthu mmodzi.
12 Ndipo mapfuko a Israyeli anatuma anthu mwa pfuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Coipa canji ici cinacitika mwa inu?
13 Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.
14 Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kucokera ku midzi kumka ku Gibeya, kuti aturuke kulimbana ndi ana a Israyeli.