1 Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israyeli, ndiwo onse amene sanadziwa nkhondo zonse za Kanani;
2 cifukwa cace ndico cokha cakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israyeli ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okha okha osaidziwa konse kale;
3 anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebano, kuyambira phiri la Baalaherimoni mpaka polowera ku Hamati.
4 Amenewo anakhala coyesera Israyeli kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ace, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.
5 Ndipo ana a Israyeli anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
6 nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao.
7 Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo.