2 Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wocita ufumu ku Hazori; kazembe wace wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.
3 Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova; pakuti anali nao magareta acitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi awiri.
4 Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wace wa Lapidoti, anaweruza Israyeli nyengo ija,
5 Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Beteli ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anakwera kwa iye awaweruze.
6 Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?
7 Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ace, ndi aunyinji ace; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.
8 Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.