10 Inu akuyenda okwera pa aburu oyera,Inu akukhala poweruzira,Ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.
11 Posamveka phokoso la amauta potunga madzi,Pomwepo adzafotokozera zolungama anazicita Yehova,Zolungama anazicita m'miraga yace, m'lsrayeli.Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.
12 Galamuka, Debora, galamuka,Galamuka, galamuka, unene nyimbo;Uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinoamu, iwe.
13 Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu;Yehova ananditsikira pakati pa acamuna.
14 Anafika Aefraimu amene adika mizu m'Amaleki;Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako.Ku Makiri kudacokera olamulira,Ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.
15 Akalonga a Isakara anali ndi Debora;Monga Isakara momwemo Baraki,Anawatuma m'cigwa namka coyenda pansi.Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikuru.
16 Wakhaliranji pakati pa makola,Kumvera kulira kwa zoweta?Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikuru.