24 Wodalitsika, woposa akazi, akhale YaeliMkazi wa Heberi Mkeni.Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema.
25 Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka,Anamtengera mafuta a mkaka m'cotengera ca mfulu.
26 Dzanja lace analitambasulira kuciciri,Ndi dzanja lace lamanja ku nyundo ya anchito,Nakhomera Sisera, nakantha mutu wace,Inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwace.
27 Pa mapazi ace anabzong'onyoka, anagwa, anagona;Pa mapazi ace anabzong'onyoka, anagwa;Pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa.
28 Anapenyerera ali pazenera, napfuulaMace wa Sisera, pa made ace,Acedweranji gareta wace?Zizengerezeranji njinga za magareta ace?
29 Akazi anzace omveka anzeru anamyankha;Koma anadziyankhira yekha mau,
30 Kodi sanapeza, sanagawa zofunkha?Namwali, anamwali awiri kwa munthu ali yense.Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga kwa Sisera;Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga, za maluwa,Nsaru za mawanga mawanga, za maluwa konse konse, kwa cofunkha ca khosi lace.