7 Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,
8 Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;
9 ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;
10 ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.
11 Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.
12 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.
13 Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.