1 Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wace, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wace, ndi kuti,
2 Nenanitu m'makutu mwa eni ace onse a ku Sekemu, Cokomera inu nciti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? mukumbukilenso kuti ine ndine wa pfuko lanu ndi nyama yanu.
3 Pamenepo abale a amace anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ace onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.
4 Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.
5 Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.