12 Ndipo ndinaceuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditaceuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;
13 ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa munthu atabvala cobvala cofikira ku mapazi ace, atamangira lamba lagolidi pacifuwa.
14 Ndipo tsitsi la pamutu pace linali loyera ngati ubweya woyera, ngati cipale cofewa; ndi maso ace ngati lawi la moto;
15 ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ace ngati mkokomo wa madzi ambiri.
16 Ndipo m'dzanja lace lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwirl; ndi m'kamwa mwace mudaturuka lupanga lakuthwa konse konse; ndipo nkhope yace ngati dzuwa lowala mu mphamvu yace.
17 Ndipo pamene ndinamuona iye, ndinagwa pa mapazi ace ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lace lamanja pa ine, nati, Usaope, ine ndine woyamba ndi wotsiriza,
18 ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.