5 Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.
6 Ndipo cinatsegula pakamwa pace kukanena zamwano pa Mulungu, kucitira mwano dzina lace, ndi cihema cace, ndi iwo akukhala m'Mwamba.
7 Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.
8 Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,
9 N gati wina ali nalo khutu, amve.
10 N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.
11 Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.