6 Ndipo cinatsegula pakamwa pace kukanena zamwano pa Mulungu, kucitira mwano dzina lace, ndi cihema cace, ndi iwo akukhala m'Mwamba.
7 Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.
8 Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,
9 N gati wina ali nalo khutu, amve.
10 N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.
11 Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.
12 Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.