13 ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.
14 Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.
15 Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali cifukwa ca kuopa cizunzo cace, nadzalira, ndi kucita cifundo;
16 nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!
17 Pakuti m'ora limodzi casanduka bwinja cuma cacikuru cotere. Ndipo watsigiro ali yense, ndi yense wakupita panyanja pakuti pakuti, ndi amarinyero, ndi onse amene amacita kunyanja, anaima patali,
18 napfuula poona utsi wa kutentha kwace, nanena, Mudzi uti ufanana ndi mudzi waukuruwo?
19 Ndipo anathira pfumbi pamitu pao, napfuula, ndi kulira, ndi kucita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, cifukwa ca kulemera kwace, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.