5 Ndipo mau anacokera ku mpando wacifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ace onse, akumuopa iye, ang'ono ndi akuru.
6 Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.
7 Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.
8 Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.
9 Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.
10 Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.
11 Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nacita nkhondo molungama.