1 Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidaeoka, ndipo kulibenso nyanja.
2 Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wace.
3 Ndipo ndinamva mau akuru ocokera ku mpando wacifumu, ndi kunena Taonani, cihema ca Mulungu ciri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ace, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;
4 ndipo adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.