14 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikaya lemba:Izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa cilengo ca Mulungu:
15 Ndidziwa nchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.
16 Kotero, popeza uti wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m'kamwa mwanga.
17 Cifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo cuma ndiri naco, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wocititsa cifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;
18 ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m'moto, kuti ukakhale wacuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadzibveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.
19 Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.
20 Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.