10 Ndipo liri nayo micira yofanana ndi ya cinkhanira ndi mbola; ndipo m'micira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.
11 Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa phompho; dzina lace m'Cihebri Abadoni, ndi m'Cihelene ali nalo dzina Apoliyoni.
12 Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso masoka awiri m'tsogolomo.
13 Ndipo mngelo wacisanu ndi cimodzi anaomba, ndipo ndinamva mau ocokera ku nyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu,
14 nanena kwa mngelo wacisanu ndi cimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pa mtsinje waukuru Pirate.
15 Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi caka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.
16 Ndipo ciwerengero ca nkhondo za apakavalo ndico zikwi makumi awiri zocurukitsa zikwi khumi; ndinamva ciwerengero cao.