8 Ndipo anali nalo tsitsi Ionga tsitsi la akazi, ndipo mano ao analingati mano a mikango.
9 Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zacitsulo; ndipo mkokomo wa: mapiko ao ngati mkokomo wa agareta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.
10 Ndipo liri nayo micira yofanana ndi ya cinkhanira ndi mbola; ndipo m'micira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.
11 Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa phompho; dzina lace m'Cihebri Abadoni, ndi m'Cihelene ali nalo dzina Apoliyoni.
12 Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso masoka awiri m'tsogolomo.
13 Ndipo mngelo wacisanu ndi cimodzi anaomba, ndipo ndinamva mau ocokera ku nyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu,
14 nanena kwa mngelo wacisanu ndi cimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pa mtsinje waukuru Pirate.