15 Yohane acita umboni za iye, napfuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; cifukwa anakhala woyamba wa ine.
16 Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo.
17 Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu.
18 Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.
19 Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayudaanatuma kwa iye ansembe ndi alembi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
20 Ndipo anabvomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Kristu.
21 Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye, Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.