4 Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.
5 Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro.
6 Cifukwa cace pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri.
7 Ndipo pambuyo pace ananena kwa akuphunzira ace, Tiyeni tipitenso ku Yudeya.
8 Akuphunzira ananena ndi iye, Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
9 Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, cifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi,
10 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, cifukwa mulibe kuunika mwa iye.