1 Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paskha, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
2 Ndipo anamkonzera iye cakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pacakudya pamodzi ndi iye.
3 Pamenepo Mariya m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a nardo a mtengo wace wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wace wa mafutawo.
4 Koma Yudase Isikariote, mmodzi wa akuphunzira ace, amene adzampereka iye, ananena,
5 Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa cifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?
6 Koma ananena ici si cifukwa analikusamalira osauka, koma cifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amabazoikidwamo.
7 Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anacisungira ici tsiku la kuikidwa kwanga.