27 Moyo wanga wabvutika tsopano; ndipo ndidzanena ciani? Atate, ndipulumutseni Ine ku nthawi iyi. Koma cifukwa ca ici ndinadzera nthawi iyi.
28 Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ocokera Kumwamba, ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.
29 Cifukwa cace khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi iye.
30 Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika cifukwa ca Ine, koma ca inu.
31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano,
32 Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.
33 Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.