34 Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?
35 Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,
36 2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.
37 Koma angakhale adacita zizindikilo zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira iye;
38 kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,3 Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulutsidwa kwa yani?
39 Cifukwa ca ici sanathe kukhulupira, pakuti Yesaya anatinso,
40 4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo ndingawaciritse.