37 Koma angakhale adacita zizindikilo zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira iye;
38 kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,3 Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulutsidwa kwa yani?
39 Cifukwa ca ici sanathe kukhulupira, pakuti Yesaya anatinso,
40 4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo ndingawaciritse.
41 5 Izi anati Yesaya, cifukwa anaona ulemerero wace; nalankhula za iye.
42 Kungakhale kotero, ambiri a mwa akuru anakhulupirira iye; koma 6 cifukwa ca Afarisi sanabvomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,
43 7 pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.