7 Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anacisungira ici tsiku la kuikidwa kwanga.
8 Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.
9 Pamenepo khamu lalikuru la Ayuda Iinadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si cifukwa: ca Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.
10 Koma ansembe akulu anapangana kuti akaphe Lazaronso;
11 pakuti ambiri a Ayuda anacoka cifukwa ca iye, nakhulupirira Yesu.
12 M'mawa mwace khamu lalikuru la anthu amene adadza kuphwando, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,
13 anatenga makwata a kanjedza, naturuka kukakomana ndi iye, napfuula, Hosana; wolemekezeka iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli.