1 Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.
2 M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.
3 Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
4 Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace.