24 Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.
25 Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.
26 Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
27 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.
28 Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.
29 Ndipo tsopano 8 ndakuuzani cisanacitike, kuti pamene citacitika mukakhulupire.
30 Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti 9 mkuru wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;