4 Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.
5 Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kucita kanthu.
6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.
7 Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu.
8 Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.
9 Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga.
10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace.