20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe.
21 Mkazi pamene akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi.
22 Ndipo inu tsono muli naco cisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu.
23 Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.
24 Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.
25 Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.
26 Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate;