1 Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ace Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeoi Inu;
2 monga mwampatsa iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa iye, awapatse iwo moyo wosatha.
3 Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.
4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza nchito imene munandipatsa ndicite.