7 Azindikira tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa Inu;
8 cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.
9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,
10 cifukwa ali anu: ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.
11 Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate. Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.
12 Pamenendinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa citayiko, kuti lembo likwaniridwe.
13 Koma tso pane ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale naco cimwemwe canga cokwaniridwa mwa iwo okha.