10 Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.
11 Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa Iupanga m'cimakecace; cikho cimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ici kodi?
12 Ndipo khamulo ndi kapitao wamkuru, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga iye,
13 nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe caka comweco.
14 Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu.
15 Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;
16 koma Petro anaima kukhomo kunja, Cifukwa cace wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anaturuka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.