14 Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu.
15 Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;
16 koma Petro anaima kukhomo kunja, Cifukwa cace wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anaturuka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.
17 Pamenepo namwali wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa akuphunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.
18 Koma akapolo ndi anyamata analikuimirirako, atasonkha mota wamakara; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.
19 Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.
20 Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.