11 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kucokera Kumwamba; cifukwa ca ici iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo cimo loposa.
12 Pa ici Pilato anafuna kumasula iye; koma Ayuda anapfuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.
13 Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,
14 Koma linali tsiku lokonza Paskha; panali monga ora lacisanu ndi cimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, Mfumu yanu!
15 Pamenepo anapfuula iwowa, Cotsani, Cotsani, mpacikeni iye! Pilato ananena nao, Ndipacike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu anayankha, Tiribe Mfumu koma Kaisara.
16 Ndipo pamenepo anampereka iye kwa iwo kutiampacike,Pamenepo anatenga Yesu;
17 ndipo anasenza mtanda yekha, naturuka kunka ku malo ochedwa Maloa-bade, amene achedwa m'Cihebri, Golgota: