32 Cifukwa cace anadza asilikari natyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopacikidwa pamodzi ndi iye;
33 koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace;
34 koma mmodzi wa asilikari anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yace, ndipo 2 panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi.
35 Ndipo 3 iye amene anaona, wacita umboni, ndi umboni wace uti woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupire.
36 Pakuti izi zinacitika, kuti lembo likwaniridwe, 4 Pfupa la iye silidzatyoledwa.
37 Ndipo linenanso lembo lina, 5 Adzayang'ana pa iye amene anampyoza.
38 6 Citatha ici. Y osefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, cifukwa ca kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Cifukwa cace anadza, nacotsa mtembo wace.