1 Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Mariya wa Magadala mamawa, kusanayambe kuca, kumanda, napenya mwala wocotsedwa kumanda.
2 Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anacotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika iye.
3 Anaturuka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda.
4 Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;
5 ndipo m'mene anawerama cosuzumira anaona nsaru zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.
6 Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsaru zabafuta zitakhala,