9 Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera iye kuuka kwa akufa.
10 Cifukwa cace akuphunzirawo anacokanso, kunka kwao.
11 Koma Mariya analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama cisuzumirire kumanda;
12 ndipo anaona angelo awiri atabvala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.
13 Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Cifukwa anacotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika iye.
14 M'mene adanena izi, anaceuka m'mbuy'o, naona Yesu ali ciriri, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.
15 Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.