20 Petro, m'mene anaceuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pacifuwa pace pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?
21 Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?
22 Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli ciani ndi iwe? unditsate Ine iwe.
23 Cifukwa cace mau awa anaturuka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli ciani ndi iwe?
24 Yemweyu ndiye wophunzira wakucita umboniza izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wace ndi woona.
25 Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.