8 Koma akuphunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.
9 Ndipo pamene anaturukira pamtunda, anapenya moto wamakara pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.
10 Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,
11 Cifukwa cace Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda Iodzala ndi nsomba zazikuru, zana limodzi, ndi makumiasanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinacuruka kotere, kokha silinang'ambika.
12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa akuphunzira anatha kumfunsa iye, Ndinu yani? podziwa kuti ndiye Ambuye.
13 Yesu anadza natenga mkate napatsa Iwo, momwemonso nsomba.
14 Imeneyo ndi nthawi yacitatu yakudzionetsera Yesu kwa akuphunzira ace, m'mene atauka kwa akufa.