14 Ndipo monga Mose anakweza njoka m'cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa;
15 kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa iye.
16 Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.
17 Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.
18 Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.
19 Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti nchito zao zinali zoipa.
20 Pakuti yense wakucita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito zace.