26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha;
27 ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.
28 Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace,
29 nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.
30 Sindikhoza kucita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; cifukwa kuti sinditsata cifuniro canga, koma cifuniro ca Iye ondituma Ine.
31 Ngati ndicita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona.
32 Wocita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene iye andicitira Ine uli woona.