23 koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;
24 cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.
25 Ndipo pamene anampeza iye tsidya lina la nyanja, anati kwa iye, Rabi, munadza kuno liti?
26 Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si cifukwa munaona zizindikilo, koma cifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
27 Gwirani nchito si cifukwa ca cakudya cimene citayika koma ca cakudya cimene citsalira ku moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera cizindikilo.
28 Pamenepo anati kwa iye, Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu?
29 Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.